Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 25:2 - Buku Lopatulika

Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Uza Aisraele apereke zopereka zao kwa Ine. Tsono iwe ulandire zoperekazo kwa munthu aliyense wa mtima wofuna kupereka.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake.

Onani mutuwo



Eksodo 25:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.


Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake.


atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu.


pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;


Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala mu Yerusalemu.


Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Ndipo choperekacho uchilandire kwa iwo ndi ichi: golide, ndi siliva, ndi mkuwa,


Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israele, limene apereka nsembe yokweza kwa Yehova, likhale cholowa chao; chifukwa chake ndanena nao, Asadzakhale nacho cholowa mwa ana a Israele.


Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.


Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a mu Israele, amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu. Lemekezani Yehova.