Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 7:16 - Buku Lopatulika

16 pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Utengenso siliva ndi golide yense amene mumpeze m'dziko lonse la Babiloni, ndiponso zopereka zimene anthu ndi ansembe adzapereka mwaufulu, mosakakamiza, kuperekera Nyumba ya Mulungu wao ya ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mutengenso siliva yense ndi golide amene mungamupeze mʼdziko lonse la Babuloni, ngakhalenso zinthu zimene anthu pamodzi ndi ansembe adzapereka mwaufulu kuperekera ku Nyumba ya Mulungu wawo ya ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 7:16
13 Mawu Ofanana  

Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.


Pamenepo akulu a nyumba za makolo, ndi akulu a mafuko a Israele, ndi akulu a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira ntchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,


Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.


Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.


Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.


Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele;


Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndi siliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.


Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.


Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa