Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 1:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Onse oyandikana nawo adaŵathandiza poŵapatsa ziŵiya zasiliva, golide, katundu, ziŵeto ndiponso mphatso zamtengowapatali, kuphatikizapo zopereka zija zimene ankazipereka mwaufulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 1:6
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.


Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndi siliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.


Ndipo pa tsiku lachinai siliva ndi golide ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uriya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Finehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Binuyi, Alevi;


Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.


Ndipo anawachitira kuti apeze nsoni pamaso pa onse amene adawamanga ndende.


Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.


Ndipo ana a Israele anachita monga mwa mau a Mose; napempha Aejipito zokometsera zasiliva, ndi zagolide, ndi zovala.


Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito, ndipo sanawakanize. Ndipo anawafunkhira Aejipito.


Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.


Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa