Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.
Eksodo 2:3 - Buku Lopatulika Koma pamene sanathe kum'bisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa mtsinje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sangathe kumubisanso, maiyo adatenga kadengu kabango, nakamata phula. Tsono mwanayo adamuika m'menemo, nakabisa kadenguko pakati pa bango lalitali m'madzi, pafupi ndi chibumi cha mtsinjewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo. |
Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.
Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.
Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m'chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja.
Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.
limene litumiza mithenga pamtsinje m'ngalawa zamagumbwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa!
Ndipo timitsinje tidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota.
Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.
Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.