Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 2:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Koma pamene sanathe kum'bisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa mtsinje.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sangathe kumubisanso, maiyo adatenga kadengu kabango, nakamata phula. Tsono mwanayo adamuika m'menemo, nakabisa kadenguko pakati pa bango lalitali m'madzi, pafupi ndi chibumi cha mtsinjewo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:3
10 Mawu Ofanana  

Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.


Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri.


Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja.


Pamenepo Farao analamulira anthu ake onse kuti, “Mwana wamwamuna aliyense akabadwa, mukamuponye mu mtsinje wa Nailo, koma wamkazi mulekeni akhale ndi moyo.”


Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo, mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi, ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro, kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala, ndi woopedwa ndi anthu. Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena. Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”


Ngalande zake zidzanunkha; ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma. Bango ndi dulu zidzafota,


mchenga wotentha udzasanduka dziwe, nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe. Pamene panali mbuto ya ankhandwe padzamera udzu ndi bango.


Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.”


Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza.


Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa