Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 2:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anam'bisa miyezi itatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anambisa miyezi itatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, adamubisa miyezi itatu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mkaziyo anatenga pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo anali wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:2
8 Mawu Ofanana  

Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.


Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.


Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.


Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi mu Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.


Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu pamaso pa Mulungu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wake:


ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwake, ndi chivomerezo cha Iye anakhala m'chitsambayo. Mdalitso ufike pamutu wa Yosefe, ndi pakati pamutu wake wa iye wokhala padera ndi abale ake.


Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akum'bala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaope chilamuliro cha mfumu.


Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa