Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 18:5 - Buku Lopatulika

Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake aamuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, paphiri la Mulungu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake amuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, pa phiri la Mulungu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yeteroyo adabwera ndi mkazi wa Mose ndi ana ake aamuna kuchipululu kuja, ku malo amene Mose adamangako mahema, pa phiri la Mulungu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa.

Onani mutuwo



Eksodo 18:5
10 Mawu Ofanana  

Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.


nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ake omwe awiri.


Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.


Pakuti anachoka ku Refidimu, nalowa m'chipululu cha Sinai, namanga tsasa m'chipululumo; ndipo Israele anamanga tsasa pamenepo pandunji paphirilo.


Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.


Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wake; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.