Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 18:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake aamuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, paphiri la Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake amuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, pa phiri la Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Yeteroyo adabwera ndi mkazi wa Mose ndi ana ake aamuna kuchipululu kuja, ku malo amene Mose adamangako mahema, pa phiri la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:5
10 Mawu Ofanana  

Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu.


Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.”


ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona.


Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo.


Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera,


Ndipo anayamba ulendo wopita ku phiri la Mulungu pamodzi ndi womuthandiza wake Yoswa.


Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu.


Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.”


Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa