Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 18:4 - Buku Lopatulika

4 ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mwana wake wachiŵiri Mose adaamutcha Eliyezere, (chifukwa adati, “Mulungu wa atate anga ndiye thandizo langa, ndipo adandipulumutsa ku lupanga la Farao.”)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:4
19 Mawu Ofanana  

Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.


Ana a Mose: Geresomo, ndi Eliyezere.


Ndi ana a Eliyezere: wamkulu ndi Rehabiya. Ndipo Eliyezere analibe ana ena, koma ana a Rehabiya anachuluka kwambiri.


Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.


Andipulumutsa kwa adani anga. Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine, mundikwatula kwa munthu wachiwawa.


Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse.


Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.


Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.


Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.


Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni.


Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.


Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.


Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.


Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midiyani; kumeneko anabala ana aamuna awiri.


Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.


nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.


Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa