ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
Eksodo 18:10 - Buku Lopatulika Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi padzanja la Aejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi pa dzanja la Aejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adati, “Mtamandeni Chauta amene adakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Farao. Mtamandeni Chauta amene adapulumutsa anthu ake ku ukapolo wa Aejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto. |
ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.
Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.
Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati,
Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ake Aisraele, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayike mau amodzi a mau ake onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wake.
Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.
Ndipo Davide anati kwa Abigaile, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine;