Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Tsono Ahimaazi adafuula kwa mfumu, kuti, “Nkwabwino!” Atatero adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu, nati, “Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wapereka m'manja mwanu anthu amene adaaukira inu mbuyanga mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Ndipo Ahimaazi anafuwula kwa mfumu, “Zonse zili bwino!” Iye anagwada pamaso pa mfumu nkhope yake atagunditsa pansi ndipo anati, “Yehova Mulungu wathu alemekezedwe! Iye wapereka mʼdzanja lathu anthu amene anawukira inu mbuye wanga mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:28
16 Mawu Ofanana  

ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.


Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.


pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.


Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.


Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.


Ndi tsiku lachinai anasonkhana m'chigwa cha Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Beraka, mpaka lero lino.


Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.


Alemekezedwe Yehova, amene sanatipereke kumano kwao tikhale chakudya chao.


Ndipo simunandipereke m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo.


Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi padzanja la Aejipito.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.


Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pabulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira,


Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa