Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:27 - Buku Lopatulika

27 Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki. Ndipo mfumu inati, Iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki. Ndipo mfumu inati, Iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Mlonda uja adati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi m'mene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu idati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Mlonda uja anati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi mmene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu inati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:27
7 Mawu Ofanana  

Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakuchipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, Iyenso abwera ndi mau.


Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.


Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimisi, pakuti ayendetsa moyaluka.


Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika, momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; atsitsimutsa moyo wa ambuyake.


Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa, momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali.


Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.


Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa