2 Samueli 18:29 - Buku Lopatulika29 Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwe ngati kutani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwa ngati kutani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Mfumu idamufunsa kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu, zinthu zamuyendera bwino?” Ahimaazi adauza mfumu kuti, “Pamene Yowabu amandituma ine, kapolo wanu, ndinaona chipiringu chachikulu cha anthu, sindikudziŵa kaya kwagwa zotani.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Mfumu inafunsa, “Kodi mnyamata uja Abisalomu watetezedwa?” Ahimaazi anayankha, “Pamene Yowabu amati azindituma ine mtumiki wanu ndinaona chipiringu cha anthu, koma sindikudziwa chinali chiyani.” Onani mutuwo |