Genesis 24:27 - Buku Lopatulika27 Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 ndipo adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene wasunga mokhulupirika lonjezo lake kwa mbuyanga. Chauta wandilondolera ine ku nyumba ya mbale wake wa mbuyanga.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 nati, “Alemekezeke Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene waonetsa kukoma mtima kwake kosasintha ndi kukhulupirika kwake kwa mbuye wanga. Yehova wanditsogolera pa ulendo wanga mpaka ndafika ku nyumba kwa abale ake a mbuye wanga.” Onani mutuwo |
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.