Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 18:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi padzanja la Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi pa dzanja la Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono adati, “Mtamandeni Chauta amene adakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Farao. Mtamandeni Chauta amene adapulumutsa anthu ake ku ukapolo wa Aejipito.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:10
16 Mawu Ofanana  

Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba amene anapereka adani ako mʼdzanja lako.” Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo.


nati, “Alemekezeke Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene waonetsa kukoma mtima kwake kosasintha ndi kukhulupirika kwake kwa mbuye wanga. Yehova wanditsogolera pa ulendo wanga mpaka ndafika ku nyumba kwa abale ake a mbuye wanga.”


Ndipo Ahimaazi anafuwula kwa mfumu, “Zonse zili bwino!” Iye anagwada pamaso pa mfumu nkhope yake atagunditsa pansi ndipo anati, “Yehova Mulungu wathu alemekezedwe! Iye wapereka mʼdzanja lathu anthu amene anawukira inu mbuye wanga mfumu.”


Ndipo inati: “Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wachita ndi dzanja lake zimene analonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide abambo anga. Pakuti Iye anati,


“Atamandike Yehova, amene wapereka mpumulo kwa anthu ake Aisraeli monga momwe analonjezera. Palibe mawu ndi amodzi omwe amene anapita pachabe pa malonjezo ake onse abwino amene anawapereka kudzera mwa mtumiki wake Mose.


Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya. Ameni ndi Ameni.


“Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.


Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.


Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu?


Alemekezedwe Mulungu, Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu. Mwachifundo chake chachikulu anatibadwitsa kwatsopano, mʼchiyembekezo chamoyo pomuukitsa Yesu Khristu kwa akufa,


Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki.


Tsono Davide anawuza Abigayeli kuti, “Alemekezeke Yehova Mulungu wa Israeli, amene wakutuma iwe lero kuti ukumane nane.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa