Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
Eksodo 17:15 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mose adamanga guwa nalitcha kuti, “Chauta ndiye mbendera yanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anamanga guwa lansembe ndipo analitcha Yehova Chipambano Changa (Yehova Nisi). |
Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.
Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.
Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.
Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wakasiya, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale laphwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu.
Pakuchiona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pake; ndipo Aroni anafuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.
Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali mu Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.