Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 24:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Apo Mose adalemba mau onse a Chauta. Ndipo adadzuka m'maŵa ndithu nayamba kumanga guwa patsinde pa phiri. Kenaka adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri ya mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena. Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 24:4
27 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.


Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pamutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamutu pake.


ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.


Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa.


Ndipo Ahiyayo anagwira chovala chake chatsopano, naching'amba khumi ndi pawiri.


Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.


Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, anaankhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisraele onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwake kwa mafuko a Israele.


Okhomera chizindikiro tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya,


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.


Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi:


Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao.


Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.


Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.


Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati padziko la Ejipito, ndi choimiritsa cha Yehova m'malire ake.


Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi.


Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.


ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;


Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele.


Ndipo Yoswa anaimika ku Giligala miyala ija khumi ndi iwiri adaitenga mu Yordani.


nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele;


Ndipo linga la mzinda linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa