Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito.
Eksodo 16:34 - Buku Lopatulika Monga Yehova analamula Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga Yehova anauza Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monga momwe Chauta adalamulira Mose, Aroni adaika mtsukowo patsogolo pa bokosi lachipangano, kuti manayo asungike. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aaroni anayika mtsuko uja pafupi ndi bokosi la Chipangano kuti manawo asungike. |
Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito.
Ndipo uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m'likasamo.
Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.
nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.
Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.
Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.
Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.
Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;
koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.
Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi kuika magome m'likasa ndinalipanga, ali m'menemo monga Yehova anandilamulira ine.