Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:50 - Buku Lopatulika

50 koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

50 koma iwe, uike Alevi asunge Kachisi wa mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula Kachisi, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

50 Uike Aleviwo kuti aziyang'anira chihema changa chaumboni, zipangizo zake ndi zonse zimene zili m'menemo. Azinyamula chihemacho, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo azichisamala. Zithando zao azimange pozungulira chihemacho.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

50 Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:50
30 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera mu Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni?


M'masiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani, ndi Yaduwa, Alevi analembedwa akulu a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariusi wa ku Persiya.


Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.


Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.


Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.


Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.


Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.


Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.


Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.


Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'chihema cha mboni.


Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele.


Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.


Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe.


Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.


kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako.


Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ake aamuna yochokera mwa ana a Israele, kuchita ntchito ya ana a Israele, m'chihema chokomanako ndi kuchita chotetezera ana a Israele; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israele, pakuyandikiza ana a Israele ku malo opatulika.


Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele anachitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a Israele anawachitira.


Ndipo atatero, Alevi analowa kuchita ntchito yao m'chihema chokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake aamuna; monga Yehova analamula Mose kunena za Alevi, momwemo anawachitira.


Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kachisi wa chihema cha umboni mu Mwamba:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa