Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.
Eksodo 15:8 - Buku Lopatulika Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutauzira mpweya wanu, madzi adaunjikana pa malo amodzi. Madzi oyenda adangoima kuti chilili, ngati khoma. Nyanja yozamayo idalimba mpaka pansi pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu madzi anawunjikana pamodzi. Nyanja yakuya ija inasanduka madzi owuma gwaa kufika pansi. |
Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.
Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere.
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka kudziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao.
Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.
Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;
Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.
pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.