Eksodo 14:3 - Buku Lopatulika Ndipo Farao adzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao adzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Farao adzaganiza kuti, ‘Aisraele asokonezeka, akungoyendayenda m'dzikomo, azingidwa ndi chipululu.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’ |
Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.
Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.
Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israele, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?
Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.
Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mzinda, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.
Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.
Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.