Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 139:2 - Buku Lopatulika

2 Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka; mumazindikira maganizo anga muli kutali.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 139:2
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pake pa Iye amene wakundiona ine?


Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako.


Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.


Koma, chifukwa cha Inu, tiphedwa tsiku lonse; tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha.


Muwerenga kuthawathawa kwanga, sungani misozi yanga m'nsupa yanu; kodi siikhala m'buku mwanu?


Yehova adziwa zolingalira za munthu, kuti zili zachabe.


Maso a Yehova ali ponseponse, nayang'anira oipa ndi abwino.


Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.


Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo anati kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israele, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu.


Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israele, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?


Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.


Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Chifukwa chanji mulinkuganizira zoipa m'mitima yanu?


Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pake, nati kwa iwo,


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa