Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 14:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Farao adzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Farao adzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Apo Farao adzaganiza kuti, ‘Aisraele asokonezeka, akungoyendayenda m'dzikomo, azingidwa ndi chipululu.’

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 14:3
15 Mawu Ofanana  

Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka; mumazindikira maganizo anga muli kutali.


Mawu asanatuluke pa lilime langa mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.


Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela


Iwo amati, “Mulungu wamusiya; mutsatireni ndi kumugwira, pakuti palibe amene adzamupulumutse.”


“Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.


Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.


“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli.


Iwo anachita zimene munakonzeratu mwachifuniro chanu ndi mphamvu yanu kuti zichitike.


Ndipo pamene masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, nyimbo iyi idzakhala mboni yanga yowatsutsa, chifukwa zidzukulu zawo sizidzayiwala nyimboyi. Ine ndikudziwa zimene iwo akulingalira kuchita, ngakhale kuti sindinawalowetse mʼdziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro.”


Anthu a ku Gaza anawuzidwa kuti, “Samsoni ali kuno!” Choncho anthuwo anazungulira malowo, kumubisalira usiku wonse ku chipata cha mzindawo. Iwo anakhala chete usiku wonse namanena kuti, “Tidzamupha mmamawa.”


Kafufuzeni ndithu malo onse kumene amabisalako, ndipo mubwerenso kuno mudzandiwuze chenicheni. Pambuyo pake ine ndidzapita nanu. Ngatidi ali mʼderalo ndidzamusaka pakati pa mabanja onse a Yuda.”


Sauli atamva kuti Davide wapita ku Keila anati, “Mulungu wamupereka kwa ine, pakuti Davide wadzitsekera yekha mʼndende polowa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi zotsekera zake.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa