Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 14:2 - Buku Lopatulika

2 Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Uza Aisraele abwerere, amange zithando patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, moyang'anana ndi Baala-Zefoni. Mumange zithando pamenepo m'mbali mwa nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 14:2
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti,


Ndipo Farao adzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera.


Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.


Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,


Nenani mu Ejipito, lalikirani mu Migidoli, lalikirani mu Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.


Chifukwa chake taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene kufikira malire a Kusi.


Ndipo ndinatulutsa atate anu mu Ejipito; ndipo munadza kunyanja; koma Aejipito analondola atate anu ndi magaleta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa