Ndipo Abimeleki anati kwa Isaki, Uchoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamphamvu wopambana ife.
Eksodo 1:9 - Buku Lopatulika Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mfumuyo idauza anthu ake kuti, “Aisraeleŵa akuchuluka kwambiri, ndipo ndi amphamvu kupambana ife. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyo inati kwa anthu ake, “Taonani, Aisraeli achuluka ndipo ndi amphamvu kwambiri kuposa ife. |
Ndipo Abimeleki anati kwa Isaki, Uchoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamphamvu wopambana ife.
Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu;
Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao.
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.
Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?