Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 8:12 - Buku Lopatulika

Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nkugwetsa pansi choonadi, ndi kuchita chifuniro chake, ndipo inakula.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nigwetsa pansi choonadi, nichita chifuniro chake, nikuzika.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Gulu lake la nkhondo linathetsa nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku; chipembedzo choonadi chinaponderezedwa pansi. Nyangayi inapambana mu zonse zimene inachita.

Onani mutuwo



Danieli 8:12
14 Mawu Ofanana  

Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao.


Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.


Ndipo musandichotsere ndithu mau a choonadi pakamwa panga; pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.


Pakuti sasamala ntchito za Yehova, kapena machitidwe a manja ake, adzawapasula, osawamanganso.


Ndipo chiweruziro chabwerera m'mbuyo, ndi chilungamo chaima patali; pakuti choona chagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


Ndipo adzabwerera kudziko lake ndi chuma chambiri; ndi mtima wake udzatsutsana ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake, ndi kubwerera kudziko lake.


Ndinapenya, ndipo nyanga yomweyi inachita nkhondo ndi opatulikawo, niwagonjetsa, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe;


Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa.


Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwagonjetsa; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.


Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.