Danieli 8:13 - Buku Lopatulika13 Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Kenaka ndinamva wina akuyankhula; ndipo woyera winanso anamufunsa kuti, “Kodi zimene ndikuziona mʼmasomphenyazi zidzatha liti? Nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku zidzakhala zoletsedwa mpaka liti? Nanga chonyansa chosokoneza chidzakhalapo mpaka liti? Kodi gulu la ankhondo lidzapondereza malo opatulika mpaka liti?” Onani mutuwo |
Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo, ndipo chikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zakuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;