Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 8:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kenaka ndinamva wina akuyankhula; ndipo woyera winanso anamufunsa kuti, “Kodi zimene ndikuziona mʼmasomphenyazi zidzatha liti? Nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku zidzakhala zoletsedwa mpaka liti? Nanga chonyansa chosokoneza chidzakhalapo mpaka liti? Kodi gulu la ankhondo lidzapondereza malo opatulika mpaka liti?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

13 Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?

Onani mutuwo Koperani




Danieli 8:13
38 Mawu Ofanana  

Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu? Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?


Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa; palibe aneneri amene atsala ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.


Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya? Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto?


Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa; mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa. Pakuti mliri woopsa udzafika, ndipo udzakugonjetsani.


Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?” Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti, “Mpaka mizinda itasanduka mabwinja nʼkusowa wokhalamo, mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo, mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,


Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa, adani athu anasakaza malo anu opatulika.


Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.


Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa, anapondereza munda wanga; munda wanga wabwino uja anawusandutsa chipululu.


“Ankhondo ake adzayipitsa linga la Nyumba ya Mulungu ndipo adzathetsa nsembe za tsiku ndi tsiku. Kenaka adzakhazikitsa chonyansa chimene chabweretsa chiwonongeko.


“Kuyambira pamene nsembe ya tsiku ndi tsiku idzathetsedwa ndi kukhazikitsa kwa chonyansa chobweretsa chisokonezo chija, padzapita masiku 1,290.


Ndinamva, koma sindinamvetsetse. Choncho ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, nanga matsiriziro a zonsezi adzakhala chiyani?”


Awa ndi masomphenya amene ine ndinaona pamene ndinali kugona pa bedi: Ndinaona, mtengo wautali kwambiri utayima pakati pa dziko lapansi.


“Ndikanali chigonere ndinaona mʼmasomphenya mngelo atayima pamaso panga, woyera, atatsika kuchokera kumwamba.


“Inu mfumu munaona mthenga woyera, akuchokera kumwamba ndipo anati, ‘Gwetsani mtengo ndipo muwuwononge, koma musiye tsinde ndi mizu yake. Tsindelo mulimange ndi unyolo wa chitsulo ndi mkuwa ndipo mulisiye pakati pa udzu wa mʼmunda. Mulole kuti linyowe ndi mame akumwamba. Likhale ngati nyama zakuthengo, mpaka zaka zidutse zisanu ndi ziwiri.’


Ndinayandikira mmodzi mwa amene anayima pamenepo ndi kumufunsa tanthauzo lenileni la zonsezi. “Kotero anandiwuza ndi kundipatsa tanthauzo la zinthu zonse izi:


“Tsono anandifotokozera kuti, ‘Chirombo chachinayi chija ndi ufumu wachinayi umene udzaoneka pa dziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu anzake onse ndipo udzawononga dziko lonse lapansi. Udzalipondaponda ndi kuliphwasula.


Adzachita pangano lolimba ndi anthu ambiri kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Koma pakatinʼpakati pa sabata limodzilo iye adzaletsa kupereka nsembe ndi chopereka. Chonyansa chosakaza chija adzachiyika mʼNyumba ya Mulungu, ndipo chidzakhalapobe mpaka wochita zimenezi atalangidwa ndi chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu.”


Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi ndi chiyani?” Iye anandiyankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu.”


Inu mudzathawa podzera mʼchigwa chapakati pa phirilo, pakuti chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa monga munachitira pa tsiku la chivomerezi nthawi ya Uziya mfumu ya Yuda. Kenaka Yehova Mulungu wanga adzabwera, pamodzi ndi oyera ake onse.


“Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira.


“Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire.


“Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri.


“Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”


“Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi.


Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.


Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.


Iye anati: “Yehova anabwera kuchokera ku Sinai ndipo anatulukira kuchokera ku Seiri; anawala kuchokera pa Phiri la Parani. Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelo kuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake.


Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.


Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?


Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.


Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira pa Adamu, ananeneratu za anthu amenewa kuti, “Onani, Ambuye akubwera ndi oyera ake osawerengeka


Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42.


Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?”


Iye anayankha kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufunsa dzina langa? Dzina laketu ndi lodabwitsa.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa