Chivumbulutso 13:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwagonjetsa; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Chidaloledwa kuŵathira nkhondo anthu a Mulungu ndi kuŵagonjetsa. Chidapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi a chilankhulo chilichonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima ndi kuwagonjetsa. Ndipo chinapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.