Danieli 2:4 - Buku Lopatulika Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu mu Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu m'Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.” |
Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.
Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya.
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu mu Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe mu Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga.
Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba mu Chiaramu, namsanduliza mu Chiaramu.
Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.
Ndipo Eliyakimu, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'chinenero cha Aramu; pakuti ife tichimva; ndipo musanene kwa ife mu Chiyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.
Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:
anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.
Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ake lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwake.
Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.
Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake.
Belitesazara iwe, mkulu wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe chinsinsi chikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwake.
Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;
Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoze kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwake.
Ndipo akulu awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariusi, mukhale ndi moyo chikhalire.
Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango.
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.