Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 4:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba mu Chiaramu, namsanduliza mu Chiaramu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba m'Chiaramu, namsanduliza m'Chiaramu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chimodzimodzinso pa nthaŵi ya Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Persiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabiyele ndi anzao ena, adalemba inanso kalata kwa Arita-kisereksesiyo. Kalatayo adailemba m'Chiaramu, ndipo poiŵerenga ankachita kutanthauzira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 4:7
12 Mawu Ofanana  

Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu mu Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe mu Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga.


Atamva tsono adani a Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israele Kachisi,


Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala mu Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Moni, ndi nthawi yakuti.


Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi, wakutsutsana naye Yerusalemu motere:


nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu,


Zolembedwa m'kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,


Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,


Ndipo napereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu.


Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse.


Ndipo Eliyakimu, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'chinenero cha Aramu; pakuti ife tichimva; ndipo musanene kwa ife mu Chiyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.


Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu mu Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.


Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu mu Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa