1 Samueli 10:24 - Buku Lopatulika24 Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Tsono Samuele adafunsa anthu onsewo kuti, “Kodi mukumuwona munthu amene Chauta wamsankha? Palibe wina wonga ameneyu pakati pa anthu onse.” Ndipo anthu onse adafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Samueli anafunsa anthu onse kuti, “Kodi mukumuona munthu amene Yehova wasankha? Palibe wofanana naye pakati pa anthu onse.” Kenaka anthu onse anafuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!” Onani mutuwo |