Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 10:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa ndipo anthu onse anamlekeza m'chifuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa anthu onse anamlekeza m'chifukwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Choncho adathamanga kukamtenga kumeneko. Ndipo ataimirira pakati pa anthu, ankaoneka wamtali, mwakuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 10:23
5 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.


Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.


Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.


Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.


Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m'chifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa