Danieli 2:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.” Onani mutuwoBuku Lopatulika4 Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu mu Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu m'Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake. Onani mutuwo |
Pamenepo Danieli, amene amatchedwa Belitesezara, anavutika mu mtima kwambiri kwa kanthawi, ndipo anasautsidwa mʼmaganizo ake. Choncho mfumu inati, “Belitesezara usalole malotowa kapena tanthauzo lake likuopse.” Belitesezara anayankha kuti, “Mbuye wanga, ndikanakonda malotowa akanakhudza adani anu okha, ndi tanthauzo lake kwa iwo okusautsani!