Amosi 2:3 - Buku Lopatulika ndipo ndidzalikha woweruza pakati pake, ndi kupha akalonga ake onse, ati Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ndidzalikha woweruza pakati pake, ndi kupha akalonga ake onse, ati Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzaŵaphera wolamulira wao, Ndidzaphanso nduna zake pamodzi naye.” Akuterotu Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzawononga wolamulira wake ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,” akutero Yehova. |
amene asandutsa akalonga kuti akhale achabe, nasandutsa oweruza a dziko lapansi akhale opanda pake.
Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.
Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.
Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;
Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.