Numeri 24:17 - Buku Lopatulika17 Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi m'Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka m'Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Ndikupenya mtsogolo, ndipo ndikuona mtundu wa Israele. Mfumu yonga nyenyezi idzatuluka mwa Yakobe, ndodo yaufumu idzadzuka mwa Israele, idzatswanya atsogoleri a Mowabu, ndipo idzagonjetseratu mtundu wa Seti. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 “Ndikumuona iye koma osati tsopano; ndikumupenya iye koma osati pafupi. Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo; ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli. Iye adzagonjetsa Mowabu ndi kugonjetsa ana onse a Seti. Onani mutuwo |