Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 24:16 - Buku Lopatulika

16 anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 munthu amene akumva mau a Mulungu, ndipo akudziŵa nzeru zake za Wopambanazonse, munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya, munthu amene akugwa pansi, koma maso ake ali chipenyere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba, amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:16
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.


Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Ndipo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;


wakumva mau a Mulungu anenetsa, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka.


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa