Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
2 Samueli 9:6 - Buku Lopatulika Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, adafika kwa Davide, adaŵerama pamaso pake, napereka ulemu. Tsono Davide adati, “Mefiboseti!” Iyeyo adayankha kuti, “Ndabwera ine mtumiki wanu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.” |
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake.
Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.
Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti.
Pamenepo mfumu Davide anatumiza anthu nakatenga iye kunyumba ya Makiri mwana wa Amiyele ku Lodebara.
Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.
Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pabulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira,