2 Samueli 9:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.” Onani mutuwoBuku Lopatulika6 Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Pamene Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, adafika kwa Davide, adaŵerama pamaso pake, napereka ulemu. Tsono Davide adati, “Mefiboseti!” Iyeyo adayankha kuti, “Ndabwera ine mtumiki wanu.” Onani mutuwo |
(Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti).