Ndipo mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye linali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao.
2 Samueli 6:17 - Buku Lopatulika Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nakalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono Davide adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. |
Ndipo mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye linali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao.
Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mzinda mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.
Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera.
Ndipo analowa nalo likasa la Mulungu, naliika pakati pa hemalo Davide adaliutsira; ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Mulungu.
Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.
Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kuchokera ku Kiriyati-Yearimu kunka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.
Ndi mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.
Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,