Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 5:6 - Buku Lopatulika

6 Ndi mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndi mfumu Solomoni ndi khamu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 5:6
6 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi chonenepa china.


Ndipo mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye linali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao.


Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwake mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe chikwi chimodzi, nkhosa zamphongo chikwi chimodzi, ndi anaankhosa chikwi chimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zochuluka za Aisraele onse:


Ndipo anakwera nalo likasa, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'chihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.


Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m'chipinda chamkati mwa Kachisi, m'malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko a akerubi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa