Levitiko 3:9 - Buku Lopatulika9 Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Tsono pa nsembe yachiyanjanoyo yopereka kwa Chauta ndi yoyenera kuitentha pa moto, atapepo mafuta onse a nkhosayo, ndiye kuti mchira wonona wathunthu, ataudula m'tsinde pafupi ndi msana, mafuta okuta matumbo, mafuta ena onse okhala pamatumbopo, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Pa nsembe yachiyanjanopo ayenera kuchotsa ndi kubweretsa: mafuta a nkhosayo, mchira wake wonse wonona atawudulira mʼtsinde pafupi ndi fupa la msana, zamʼkati zonse ndi mafuta onse amene akuta ziwalo zamʼkatimo, Onani mutuwo |
Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pake pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidachepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.