Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.
2 Samueli 3:3 - Buku Lopatulika wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wachiŵiri anali Kiliyabu, wobadwa kwa Abigaile, mkazi wamasiye wa Nabala, wa ku Karimele. Wachitatu anali Abisalomu, wobadwa kwa Maaka, mwana wa Talimai, mfumu ya ku Gesuri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli. Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri; |
Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.
Ndipo mfumu inati, Apatukire kunyumba ya iye yekha, koma asaone nkhope yanga. Chomwecho Abisalomu anapatukira kunyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.
Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.
Ndipo kunali pakutha zaka zinai Abisalomu ananena kwa mfumu, Mundilole ndimuke ku Hebroni ndikachite chowinda changa ndinachiwindira Yehova.
Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri mu Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova.
Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!
Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele.
Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.
Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisraele onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Yehova.
Ana a Davide tsono ombadwira ku Hebroni: woyamba Aminoni wa Ahinowamu wa ku Yezireele, wachiwiri Daniele wa Abigaile wa ku Karimele,
wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wachinai Adoniya mwana wa Hagiti,
Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).
Koma ana a Israele sanainge Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israele, mpaka lero lino.
Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.
Ndipo Abigaile anafulumira nanyamuka, nakwera pabulu, pamodzi ndi anamwali ake asanu akumtsata; natsatira mithenga ya Davide, nakhala mkazi wake.
Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.