2 Samueli 18:33 - Buku Lopatulika33 Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga! Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga! Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa33 Pamenepo mfumu idagwidwa ndi chisoni chachikulu, nikwera ku chipinda cham'mwamba pa chipata kukalira. Tsono popita inkati, “Iwe mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu. Kalanga ine, achikhala ndidaafa ndine m'malo mwako! Iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Mfumu inanthunthumira. Inapita ku chipinda cha mmwamba cha pa chipata kukalira. Pamene imapita, inkati: “Iwe mwana wanga Abisalomu! Mwana wanga! Mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine mʼmalo mwako! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!” Onani mutuwo |