Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukuchitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukuchitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tsono mfumuyo idafunsa Mkusi uja kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu zinthu zamuyendera bwino?” Mkusiyo adayankha kuti, “Adani anu mbuyanga mfumu, pamodzi ndi anthu onse amene amakuukirani, ziŵaonekere zomwe zamuwonekera mwanayo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Mfumu inafunsa Mkusiyo kuti, “Kodi mnyamata uja Abisalomu watetezedwa?” Mkusiyo anayankha kuti, “Adani anu mbuye wanga mfumu, pamodzi ndi anthu onse amene amakuwukirani, ziwaonekere zomwe zamuonekera mnyamatayo.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:32
8 Mawu Ofanana  

Pamenepo Yowabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yowabu, nathamanga.


Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwe ngati kutani.


Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.


Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, ndipo zimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri.


Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.


Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.


Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa