Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Mkusi uja nayenso adafika, ndipo adati, “Ndakutengerani uthenga wabwino, mbuyanga mfumu. Lero lino Chauta wakupulumutsani ku mphamvu za anthu onse amene ankakuukirani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Kenaka Mkusi uja anafika ndipo anati, “Mbuye wanga mfumu imvani nkhani yabwino! Yehova wakupulumutsani inu lero kwa onse amene anakuwukirani.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:31
11 Mawu Ofanana  

Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera chilango adani ake.


Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.


Ndipo mfumu inati, Patuka nuime apa. Napatuka, naimapo.


Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.


Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.


Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa