2 Samueli 3:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli. Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri; Onani mutuwoBuku Lopatulika3 wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Wachiŵiri anali Kiliyabu, wobadwa kwa Abigaile, mkazi wamasiye wa Nabala, wa ku Karimele. Wachitatu anali Abisalomu, wobadwa kwa Maaka, mwana wa Talimai, mfumu ya ku Gesuri. Onani mutuwo |
Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’ ”