Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:3 - Buku Lopatulika

3 Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Munthuyo anali Nabala, wa fuko la Kalebe, ndipo mkazi wake anali Abigaile. Mkaziyo anali wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wakeyo anali wouma mtima ndi wankhanza. Anali wa fuko la Kalebe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Dzina lake linali Nabala ndipo anali wa fuko la Kalebe. Dzina la mkazi wake linali Abigayeli. Anali mkazi wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wake, wa banja la Kalebe, anali wowuma mtima ndi wamwano pa zochita zake.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anayandikira kulowa mu Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;


Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.


Mkazi yense wanzeru amanga banja lake; koma wopusa alipasula ndi manja ake.


Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.


chifukwa cha kapolo pamene ali mfumu; ndi chitsiru chitakhuta zakudya;


Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale.


Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.


Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.


Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.


Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaone anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza.


Ndipo Davide anamva kuchipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zake.


Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa