Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo atate wake sadamvuta masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Bambo wake Davide anali asanamdzudzulepo nkamodzi komwe pomufunsa kuti, “Kodi zakutizakutizi ukuchitiranji?” Adoniyayo anali wokongola, ndipo adaapondana ndi Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 (Abambo ake sanalowererepo nʼkamodzi komwe ndipo sanafunsepo kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?” Adoniyayo anali wokongola kwambiri ndipo anali wopondana ndi Abisalomu).

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:6
11 Mawu Ofanana  

Ndipo mu Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pamutu wake mwa iye munalibe chilema.


Ndipo mfumu Solomoni anayankha, nati kwa amai wake, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wake wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkulu wanga; inde ukhale wake, ndi wa Abiyatara wansembeyo, ndi wa Yowabu mwana wa Zeruya.


wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wachinai Adoniya mwana wa Hagiti,


Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.


Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.


Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa ndipo anthu onse anamlekeza m'chifuwa.


Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.


Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m'chifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa