Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo kunali pakutha zaka zinai Abisalomu ananena kwa mfumu, Mundilole ndimuke ku Hebroni ndikachite chowinda changa ndinachiwindira Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo kunali pakutha zaka zinai Abisalomu ananena kwa mfumu, Mundilole ndimuke ku Hebroni ndikachite chowinda changa ndinachiwindira Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Patapita zaka zinai, Abisalomu adapempha mfumu kuti, “Chonde mundilole kuti ndipite ku Hebroni kuti ndikachite zimene ndidalumbira kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Patapita zaka zinayi Abisalomu anati kwa mfumu, “Loleni ndipite ku Hebroni kuti ndikakwaniritse lonjezo limene ndinachita kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:7
10 Mawu Ofanana  

Chomwecho anathawa Abisalomu, nanka ku Gesuri, nakakhala kumeneko zaka zitatu.


Ndipo ana a Davide anabadwira ku Hebroni. Mwana woyamba ndiye Aminoni, wa Ahinowamu wa ku Yezireele;


wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;


Nsembe ya oipa inyansa; makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.


Taonani, inu musala kudya kuti mukangane ndi kutsutsana ndi kukantha ndi nkhonya yoipa; inu simusala kudya tsiku lalero kuti mumveketse mau anu kumwamba.


Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa